
| Investigating Bilingual Literacy: Evidence from Malawi and Zambia - Education research paper No. 24 (DFID, 1998, 99 p.) |
Mfumu Mitulo atacoka pamudzi paja nyakwawa Kameta ndi anthu ake pamodzi ndi ena ocokera m'midzi yozungulira, anagundika nayo nchito youmba ncherwa zomangira sukulu.
Azimai ndiwo amabweretsa madzi ndi udzu wophimba pancherwa, pamene anyamata anali kuthamanga ndi zikombole. Azibambo ndiwo anali m'nkhando kumaponda dothi. Panthawiyi amuna ena anali kudula nkhuni zodzatenthera ncherwa.
Ncherwa zittakonzedwa, nyakwawa Kameta anauza Bambo Jamu omwe
amadziwa kamangidwe ke nyumba za ncherwa kuti akayambeko kukumba maziko a
sukulu.